Leviticus 23:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka chilichonse, masiku asanu ndi aŵiriwo musamale kuti akhale achikondwerero, olemekeza Chauta. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibadwo yonse. Muzilisunga pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo musunge chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri m'chaka; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; musunge mwezi wachisanu ndi chiwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chaka chilichonse muzichita chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse. Muzichita chikondwerero chimenechi mwezi wachisanu ndi chiwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo muwasunge madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri m'caka; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; musunge mwezi wacisanu ndi ciwiri.