Leviticus 23:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mupereke nsembe yopsereza kwa Chauta pa masiku asanu ndi aŵiri. Tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku la msonkhano wopatulika, musagwire ntchito zotopetsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lachisanu ndi chiwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito yolemetsa.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lacisanu ndi ciwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.