Leviticus 24:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu uja adanyoza dzina la Chauta ndi kulitemberera. Tsono adabwera naye kwa Mose. Dzina la mai wake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele anachitira Dzina mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wake ndiye Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu uja ananyoza dzina la Yehova ndi kulitemberera. Choncho anabwera naye kwa Mose. Dzina la amayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mwana wamwamuna wa mkazi M-israyeli anacitira DZINA mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wace ndiye Selomiti, mwana wa Dibri, wa pfuko la Dani.