Leviticus 24:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Umtulutse kuzithandoko munthu wotembererayo. Onse amene adamumva akutemberera asanjike manja ao pamutu pake, kutsimikiza kuti ndi wochimwadi, ndipo mpingo wonse umponye miyala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tuluka naye wotembererayo kunja kwa chigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pake, ndi khamu lonse limponye miyala afe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pita naye kunja kwa msasa munthu wotembererayo. Onse amene anamumva akutemberera asanjike manja awo pamutu pake ndipo gulu lonse la anthu limugende miyala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Turuka naye wotembererayo kunja kwa cigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pace, ndi khamu lonse limponye miyala afe.