Leviticus 24:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
wonyoza dzina la Chauta ayenera kuphedwa. Mpingo wonse umponye miyala. Mlendo kapena mbadwa akangonyoza dzina la Chauta, ayenera kuphedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi iye wakuchitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akachitira dzina la Yehova mwano, awaphe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense wonyoza dzina la Yehova, mlendo ngakhale mbadwa, aphedwe. Gulu lonse la anthu limuponye miyala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi iye wakucitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akacitira dzina la Yehova mwano, awaphe.