Leviticus 24:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aroni aiyatse nyaleyo pamaso pa Chauta kunja kwa nsalu yochinga bokosi lachipangano, limene lili m'chihema chamsonkhano, kuti ikhale chiyakire kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. Limeneli likhale lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aroni aikonze kunja kwa nsalu yotchinga ya mboni, m'chihema chokomanako, kuyambira madzulo kufikira m'mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunja kwa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano, mʼchihema cha msonkhano, Aaroni azionetsetsa kuti nyale ikukhala chiyakire pamaso pa Yehova kuyambira madzulo mpaka mmawa, nthawi zonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aroni aikonze kunja kwa nsaru yocinga ya mboni, m'cihema cokomanako, kuyambira madzulo kufikira m'mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu.