Leviticus 24:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chakudyacho chikhale cha Aroni ndi ana ake, ndipo achidyere m'malo oyera, pakuti kwa iyeyo chimenecho nchopatulika kopambana, chochokera pa nsembe yopsereza kwa Chauta. Lamuloli ndi lamuyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ake, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulika kwambiri wochokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chakudyacho ndi cha Aaroni ndi ana ake ndipo azidyera ku malo wopatulika chifukwa kwa iye chakudyacho ndi chopatulika kwambiri chochokera pa chopereka chopsereza cha Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ace, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulikitsa wocokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.