Leviticus 25:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mupatule chaka cha 50, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu m'dziko lonselo kwa onse amene ali m'menemo. Kwa inu chaka chimenecho chidzakhale chokondwerera zaka 50, pamene aliyense adzayenera kubwerera pa mtunda wake, ndipo aliyense mwa inu abwerere ku banja lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo muchipatule chaka cha makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m'dzikomo kuti akhale aufulu; muchiyese chaka choliza lipenga; ndipo mubwerere munthu aliyense ku zakezake, ndipo mubwerere yense ku banja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mupatule chaka cha makumi asanu, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu mʼdziko lonse kwa onse amene ali mʼmenemo. Kwa inu chakachi chidzakhala choyimba lipenga la chikondwerero. Aliyense wa inu adzayenera kubwerera pa munda wake, ndipo aliyense wa inu adzabwerera ku fuko lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mucipatule caka ca makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m'dzikomo kuti akhale aufulu; muciyese caka coliza lipenga; ndipo mubwerere munthu ali yense ku zace zace, ndipo mubwerere yense ku banja lace.