Leviticus 25:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ugule kwa mnzako potsata chiŵerengero cha zaka zimene zidapita kuyambira pa chikondwerero cha chaka cha 50 chapita. Ndipo mnzakoyo akugulitse potsata chiŵerengero cha zaka zokolola zimene zatsala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga mwa kuwerenga kwake kwa zaka, chitapita choliza lipenga, uzigula kwa mnansi wako, ndi monga mwa kuwerenga kwa zaka za zipatso azigulitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ugule kwa mnzako potsata chiwerengero cha zaka zimene zatha kuyambira pa chikondwerero cha chaka cha makumi asanu chapita. Ndipo mnzakoyo akugulitse potsata chiwerengero cha zaka zokolola zomwe zatsala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga mwa kuwerenga kwace kwa zaka, citapita coliza lipenga, uzigula kwa mnansi wako, ndi monga mwa kuwerenga kwa zaka za zipatso azigulitsa.