Leviticus 25:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zaka zikachuluka uwonjezere mtengo, zaka zikachepa uchepetse mtengo, poti akukugulitsani potsata chiŵerengero cha zaka zokolola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga mwa kuchuluka kwa zaka zake uonjeze mtengo wake, ndi monga mwa kuchepa kwa zaka zake uchepse mtengo wake; pakuti akugulitsa powerenga masiku ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zaka zikakhala zochuluka, uwonjezere mtengo, ndipo zaka zikakhala zochepa, uchepetse mtengo, pakuti chimene iye akukugulitsa ndi zaka zokolola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga mwa kucuruka kwa zaka zace uonjeze mtengo wace, ndi monga mwa kucepa kwa zaka zace ucepse mtengo wace; pakuti akugulitsa powerenga masiku ace.