Leviticus 25:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu akakhala wopanda mbale woti aombole mtundawo, ndipo pambuyo pake munthuyo nkusanduka wolemera, napeza zokwanira kuti auwombole,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu akasowa mombolo, koma dzanja lake lachionetsa, nachipeza chofikira kuchiombola;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati munthuyo alibe wachibale woti nʼkuwombola malowo koma pambuyo pake iye mwini nʼkulemera ndi kupeza zokwanira kuwombolera, awombole malowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu akasowa mombolo, koma dzanja lace lacionetsa, nacipeza cofikira kuciombola;