Leviticus 25:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma akapanda kukhala nazo zokwanira zoti aombolere, mtundawo udzakhalebe m'manja mwa amene adagulayo, mpaka pa chaka chokondwerera zaka 50. Pa chaka chimenecho mtundawo udzakhala woombola ndipo ubwerere kwa mwiniwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma dzanja lake likapanda kupeza zofikira za kumbwezera, pamenepo chogulitsacho chikhale m'dzanja lake la iye adachigulayo, kufikira chaka choliza lipenga; koma chaka choliza lipenga chituluke, nabwerere iye ku dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati sakhala nazo zokwanira kuti amubwezere amene anagula malowo, gawo limene anagulitsalo lidzakhala mʼmanja mwa munthu amene anagulayo mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Malowo adzabwezedwa chaka chimenechi, ndipo iye adzatha kubwerera pa malo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma dzanja lace likapanda kupeza zofikira za kumbwezera, pamenepo cogulitsaco cikhale m'dzanja lace la iye adacigulayo, kufikira caka coliza lipenga; koma caka coliza lipenga cituruke, nabwerere iye ku dziko lace.