Leviticus 25:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu akagulitsa nyumba ya mu mzinda wozingidwa ndi linga, angathe kuiwombola chisanathe chaka chathunthu ataigulitsa. Adzatha kuiwombola pa nthaŵi yomweyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akagulitsa nyumba yogonamo, m'mudzi wa m'linga, aiombole chisanathe chaka choigulitsa; kufikira kutha chaka akhoza kuombola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthu agulitsa nyumba ya mu mzinda umene uli mu linga, angathe kuyiwombola nyumbayo chisanathe chaka chathunthu chigulitsire. Mu nthawi imeneyi wogulitsayo atha kuyiwombola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akagulitsa nyumba yogonamo, m'mudzi wa m'linga, aiombole cisanathe caka coigulitsa; kufikira kutha caka akhoza kuombola.