Leviticus 25:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyumbayo ikapanda kuwomboledwa chisanathe chaka chimodzicho, nyumba ya mu mzinda wozingidwa ndi malingawo idzakhala ya munthu amene adagulayo pa mibadwo yake yonse. Sidzaomboledwa pa chaka chokondwerera zaka 50.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akapanda kuiombola kufikira kutha kwake kwa chaka champhumphu, nyumba ili m'mudzi wa m'lingayi idzakhala yake ya iye adaigula yosamchokeranso mwa mibadwo yake; siidzatuluka chaka choliza lipenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati nyumbayo siwomboledwa chisanathe chaka chimodzicho, nyumbayo idzakhala ya amene anagulayo ndi zidzukulu zake mpaka muyaya. Sidzabwezedwanso kwa mwini wake mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akapanda kuiombola kufikira kutha kwace kwa caka camphumphu, nyumba iri m'mudzi wa m'lingayi idzakhala yace ya iye adaigula yosamcokeranso mwa mibadwo yace; siidzaturuka caka coliza lipenga.