Leviticus 25:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma nyumba zam'midzi, zosazingidwa ndi malinga, achite nazo monga momwe amachitira ndi minda yam'dzikomo. Angathe kuziwombola, ndipo zibwezedwe pa chaka chokondwerera zaka 50.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma nyumba za m'midzi yopanda linga aziyese monga minda ya m'dziko; ziomboledwe, zituluke m'chaka choliza lipenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma nyumba za mʼmizinda yosazingidwa ndi linga ziwomboledwe monga mmene achitira ndi minda ya mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma nyumba za m'midzi yopanda linga aziyese monga minda ya m'dziko; ziomboledwe, zituruke m'caka coliza lipenga.