Leviticus 25:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usalandire chiwongoladzanja pa ndalama zimene adakongola, kapena kuwonjezerapo zina, koma uziwopa Mulungu wako, ndipo ulole mbale wakoyo kuti akhale nawe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usamambwezetsa phindu, kapena chionjezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usalandire chiwongoladzanja chilichonse kuchokera kwa iye kapena kuwonjezerapo kanthu kena, koma uziopa Mulungu kuti mʼbale wakoyo akhale nawe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usamambwezetsa phindu, kapena cioniezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.