Leviticus 25:50 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aŵerengerane ndi munthu adamgulayo kuyambira chaka chimene adadzigulitsa kwa iyeyo mpaka chaka chokondwerera zaka 50. Mtengo wa kuwomboledwa kwake ukhale wolingana ndi chiŵerengero cha zakazo. Nthaŵi imene anali ndi mbuyakeyo iŵerengedwe monga ngati nthaŵi ya munthu wantchito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira chaka adadzigulitsa kwa iye kufikira chaka choliza lipenga; ndipo mtengo wake ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye pamodzi ndi munthu amene anamugulayo awerengerane kuyambira chaka chimene anadzigulitsa kwa iyeyo mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Mtengo wodziwombolera ukhale wofanana ndi zakazo. Ndipo nthawi imene anali ndi mbuye wakeyo iwerengedwe ngati nthawi ya munthu wantchito.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira caka adadzigulitsa kwa iye kufikira caka coliza lipenga; ndipo mtengo wace ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.