Leviticus 25:52 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zikangotsala zaka zoŵerengeka kuti chifike chaka chokondwerera zaka 50, aŵerengerane ndi mbuye wake, ndipo potsata zaka zotsala mpaka cha 50, abweze ndalama za kuwomboledwa kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zikamtsalira zaka pang'ono kufikira chaka choliza lipenga amwerengere; monga mwa zaka zake abwezere mtengo wake wakumuombola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati kwatsala zaka zochepa kuti ifike nthawi ya chaka chokondwerera zaka makumi asanu, iye awerengerane ndi mbuye wake, ndipo apereke ndalama za zowomboledwera molingana ndi zaka zotsalazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zikamtsalira zaka pang'ono kufikira caka coliza lipenga amwerengere; monga mwa zaka zace abwezere mtengo wace wakumuombola.