Leviticus 25:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muziŵerenga masabata asanu ndi aŵiri a zaka, zaka zisanu ndi ziŵiri kuchulukitsa kasanunkaŵiri, kuti nyengo ya masabata asanu ndi aŵiri a zakayo ikwanire zaka 49 pamodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Muzichotsera Masabata asanu ndi awiri a zaka, ndi kuchulukitsa zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawirinso kuti Masabata asanu ndi awiri a zakawo akwane zaka 49.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai.