Leviticus 26:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Musadzipangire mafano ndipo musaimike zithunzi zosema kapena miyala yachipembedzo. Musaimiritse miyala yosema mwachithunzi m'dziko mwanu kuti muziipembedza. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umene; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena coimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umene; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.