Leviticus 26:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo a Aejipito. Ndadula goli lanu kuti muziyenda moongoka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinathyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani choweramuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinatyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani coweramuka.