Leviticus 26:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndidzakuchitani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi, chifuwa chachikulu choondetsa ndiponso malungo oononga maso ndi ofooketsa moyo. Mudzabzala mbeu zanu, koma osakololapo kanthu, chifukwa choti adani anu adzazidya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m'chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzakuchitirani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi monga chifuwa chachikulu chowondetsa ndiponso malungo amene adzawononga maso ndi kufowoketsa moyo wanu. Mudzangovutika kudzala mbewu zanu chifukwa adani anu adzazidya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndidzacitira inu icinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthendayoondetsayam'cifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu cabe, pope za adani anu adzazidya.