Leviticus 26:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaononga nyonga zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale youma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza ndidzathyola mphamvu yanu yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati chitsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzathyola mphamvu zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale yowuma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza ndidzatyola mphamvu yam yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati citsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;