Leviticus 26:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzabweretsanso zilombo zolusa pakati panu, zimene zidzakudyerani ana anu, ndi kukuwonongerani ng'ombe zanu. Zilombozo zidzachepetsa chiŵerengero chanu, kotero kuti m'njira zanu simuzidzapita anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza ndidzatumiza chilombo cha kuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu nichidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzabweretsa zirombo zolusa pakati panu, ndipo zidzakulandani ana anu ndi kuwononga ngʼombe zanu. Choncho zidzachepetsa chiwerengero chanu kotero kuti mʼnjira mwanu simudzapita anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza ndidzatumiza cirombo ca kuthengo pakati pa inu, ndipo cidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu nicidzacepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.