Leviticus 26:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzabweretsa lupanga pa inu limene lidzakulangani chifukwa chophwanya chipangano changa. Ndipo mukasonkhana m'mizinda mwanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani m'manja mwa adani anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'midzi mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndidzabweretsa lupanga pa inu ndi kukulangani chifukwa chophwanya pangano langa. Mukadzasonkhana mʼmizinda yanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani mʼmanja mwa adani anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakucita cilango ca cipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'midzi mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.