Leviticus 26:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa nyengo imeneyo nthaka idzakondwerera zaka zoipumitsa nthaŵi yonse pamene m'dzikomo mulibe anthu, inu muli m'dziko la adani anu. Pamenepo nthaka idzapuma ndi kukondwerera zaka zopumazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ake, masiku onse a kupasuka kwake, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo nthaka idzasangalalira kuyipumitsa kwake nthawi yonse imene idzakhala yosalimidwa, pamene inu mudzakhala muli mʼdziko la adani anu. Pa nthawi imeneyo dziko lidzapumula ndi kukondwerera kulipumuza kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ace, masiku onse a kupasuka kwace, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ace.