Leviticus 26:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ngakhale ena amene mudzatsalenu, ndidzaika mtima wa mantha mwa inu pamene muli m'dziko la adani anu. Mtswatswa wa tsamba louluka udzakuthaŵitsani. Mudzathaŵa monga m'mene munthu amathaŵira lupanga, ndipo mudzagwa pansi popanda okuthamangitsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Kunena za amene adzatsale, ndidzayika mantha mʼmitima mwawo mʼdziko la adani awo kotero kuti adzathawa ngakhale mtswatswa wa tsamba lowuluka ndi mphepo. Adzathawa ngati akuthawa lupanga, ndipo adzagwa pansi ngakhale padzakhale wopanda kuwapirikitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapitikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.