Leviticus 26:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ayambe aisiya nthaka yaoyo, kuti ikondwerere zaka zoipumuza, pamene dziko lili lopanda anthu, iwo atachoka. Tsono iwo adzalangika chifukwa cha machimo ao, popeza kuti adanyoza zimene ndidaŵalamula, ndipo mitima yao idadana ndi malangizo anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ake, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzavomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti adzasiya dziko lawo lopanda anthu, nthaka idzakondwerera zaka zake zoyipumuza pamene iwo kudzakhala kulibe. Koma adzalangidwa chifukwa cha machimo awo popeza anakana malamulo anga ndipo mitima yawo inkayipidwa nawo malangizo anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ace, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzabvomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.