Leviticus 26:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzakhala mukupuntha dzinthu mpaka nthaŵi yothyola zipatso, ndipo mudzakhala mukuthyola zipatso mpaka nthaŵi yobzala. Mudzadya chakudya mpaka kukhuta, ndi kumakhala m'dziko mwanu popanda chokuvutani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mudzakhala mukupuntha tirigu mpaka nthawi yothyola mphesa, ndipo mudzakhala mukuthyola mphesa mpaka nthawi yodzala. Mudzadya chakudya chanu mpaka kukhuta ndipo mudzakhala mʼdziko lanu mwamtendere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yochera mphesa, ndi nyengo yochera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta naco cakudya canu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.