Leviticus 27:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pamene munthu apereka nyumba yake kuti ikhale yopatulikira Chauta, wansembe aiwone ngati ili yabwino kapena ai. Monga momwe wansembe aiwonere, idzakhala momwemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akapatula nyumba yake ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe aziiyesa mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga wansembeyo aiyesa, ikhale momwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthu apereka nyumba yake kuti ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe atchule mtengo wake poona ngati ndi yabwino kapena ndi yoyipa. Mtengo umene wansembe atchule ndiwo udzakhale mtengo wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akapatula nyumba yace ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe aziiyesa mtengo wace, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga wansembeyo aiyesa, ikhale momwemo.