Leviticus 27:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu akapereka kwa Chauta chigawo cha dera la choloŵa chake, mtengo umene uike ukhale wolingana ndi mbeu zodzabzalamo. Pa mbeu za barele zokwanira makilogaramu 20, mtengo wake ukhale wokwana mashekeli asiliva 50.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akapatulirako Yehova munda wakewake, uziuyesa monga mwa mbeu zake zikakhala; homeri wa barele uuyese wa masekeli makumi asanu a siliva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthu apereka kwa Yehova mbali ina ya malo a makolo ake, mtengo umene awuyike ukhale wolingana ndi mtengo wa mbewu zimene zimadzabzalidwamo. Zikhale mbewu za barele za makilogalamu makumi awiri ndipo mtengo wake ukhale masekeli makumi asanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akapatulirako Yehova munda wace wace, uziuyesa monga mwa mbeu zace zikakhala; homeri wa barie uuyese wa masekeli makumi asanu a siliva.