Leviticus 27:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma akapereka munda wake chitatha chaka chokondwerera zaka 50, wansembe aŵerenge mtengo wa ndalama molingana ndi zaka zotsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka 50, ndipo achotse pa mtengo umene wansembe waika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akaupatula munda wake chitapita chaka choliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira chaka choliza lipenga, nazichepsako pa kuyesa kwako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati apereka mundawo chaka chokondwerera zaka makumi asanu chitapita, wansembe adzatchula mtengo molingana ndi zaka zomwe zatsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka makumi asanu, ndipo mtengo wake udzakhala wotsikirapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akaupatula munda wace citapita caka coliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira caka coliza lipenga, nazicepsako pa kuyesa kwako.