Leviticus 27:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwini mundawo atausiya pa chaka chokondwerera zaka 50, udzakhala wopatulikira Chauta ngati munda woperekedwa. Wansembe adzautenga kuti ukhale wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma potuluka m'chaka choliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; ukhale wakewake wa wansembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwini mundawo akawusiya mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu ndiye kuti mundawo udzakhala wopatulika monga woperekedwa kwa Yehova: udzakhala munda wa ansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma poturuka m'caka coliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa ciperekere kwa Mulungu; ukhale wace wace wa wansembe.