Leviticus 27:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma chinthu chilichonse choperekedwa kwathunthu kwa Chauta, kaya ndi munthu kapena nyama kapena munda umene uli choloŵa chake, chisagulitsidwe kapena kuwomboledwa. Chinthu chilichonse choperekedwa choncho kwa Chauta, nchopatulika kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma asachigulitse kapena kuchiombola chinthu choperekedwa chiperekere kwa Mulungu, chimene munthu achipereka chiperekere kwa Yehova, chotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wakewake; chilichonse choperekedwa chiperekere kwa Mulungu nchopatulika kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma chinthu chilichonse choperekedwa kwa Yehova, kaya ndi munthu, nyama, kaya ndi malo a makolo, chimenechi chisagulitsidwe kapena kuwomboledwa. Choperekedwa kwa Yehova motere nʼchopatulika kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma asacigulitse kapena kuciombola cinthu coperekedwa ciperekere kwa Mulungu, cimene munthu acipereka ciperekere kwa: Yehova, cotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wace wace; ciri conse coperekedwa ciperekere kwa Mulungu neopatulikitsa.