Leviticus 27:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo chigawo chachikhumi chilichonse cha nsambi wa ng'ombe ndi wa nkhosa, ndiye kuti nyama yachikhumi iliyonse imene mbusa aiŵerenge, ikhale yopatulikira Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo limodzi la magawo khumi lonse la ng'ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi, zilizonse zimapita pansi pa ndodo, limodzi la magawo khumi likhala lopatulikira Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chakhumi cha ngʼombe ndi nkhosa, kapena kuti nyama iliyonse ya khumi imene mʼbusa wayiwerenga idzakhala yopatulikira kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo limodzi la magawo khumi lonse la ng'ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi, ziri zonse zimapita pansi pa ndodo, limodzi la magawo khumi likhale lopatulikira Yehova.