Leviticus 27:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu akakhala wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira mtengo umenewo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo aike mtengo pa iye. Mtengo umene wansembeyo aike ukhale wolingana ndi momwe munthu wolumbirayo angalipire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma chuma chake chikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati munthu amene anachita lumbiro ndi wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira ndalama zimenezo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayike mtengo woti munthu wolumbirayo angathe kulipira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma cuma cace cikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.