Leviticus 4:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kungoti ng'ombe yonseyo, atuluke nayo kunja kwa mahema, ku malo oyeretsedwa kumene amatayako phulusa, ndipo pamalo pomwepo aitenthere pa moto wankhuni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
inde ng'ombe yonse, kunja kwa chigono, kunka nayo kumalo koyera, kumene atayako mapulusa, naitenthe pankhuni ndi moto; aitenthe potayira mapulusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kapena kuti ngʼombe yonse yotsalayo apite nayo kunja kwa msasa ku malo woyeretsedwa, kumene amatayako phulusa ndi kuyitentha pa nkhuni, pa phulusapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
inde ng'ombe yonse, kunja kwa cigono, kumka nayo kumalo koyera, kumene atayako mapulusa, naitenthe pankhuni ndi moto; aitenthe potayira mapulusa.