Leviticus 4:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ngati mpingo wonse wa Aisraele uchimwa mosachitira dala, nuchita zimene Chauta amaletsa, ngakhale uli wosadziŵako, ngwopalamula ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo khamu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati gulu lonse la Aisraeli lichimwa mosadziwa, nachita chomwe ndi choletsedwa ndi Yehova, ngakhale kuti gulu lonselo silikudziwa kuti lachimwa, anthuwo ndi olakwa ndithu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo khamu lonse la Israyeli likalakwa osati dala, ndipo cikabisika cinthuci pamaso pa msonkhano, litacita cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Yehova, ndi kuparamula;