Leviticus 4:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Umu ndimo m'mene ng'ombe yamphongo aichitire. Monga adachitira ndi ng'ombe yamphongo yopereka pa nsembe yopepesera machimo, ndimo aichitirenso imeneyi. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimowu, mpingowo udzakhululukidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anachitira ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo wansembe awachitire chowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo achite ndi ngʼombe yayimunayi monga anachitira ndi ngʼombe yayimuna yopepesera machimo. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera anthu, ndipo machimo awo adzakhululukidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anacitira ng'ombe ya nsembe yaucimo; ndipo wansembe awacitire cowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.