Leviticus 4:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
tchimo lakelo akalizindikira, apereke nsembe ya mbuzi yaikazi yopanda chilema, chifukwa cha tchimo lakelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake mbuzi yaikazi, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati wauzidwa za tchimo limene wachita, abweretse mbuzi yayikazi yopanda chilema kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace mbuzi yaikazi, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita.