Leviticus 4:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
wochimwayo akakhala wansembe wodzozedwa, pakutero wausandutsa wopalamula mpingo wonse, tsono azipereka kwa Chauta ng'ombe yaing'ono yamphongo yopanda chilema, chifukwa cha tchimo lakelo. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati wansembe wodzozedwa achimwa, ndi kuchimwitsa anthu onse, iyeyu ayenera kupereka mwana wangʼombe wamphongo wopanda chilema chifukwa cha tchimo limene wachitalo. Imeneyi ndi nsembe ya Yehova yopepesera tchimo lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kuparamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita, ikhale nsembe yaucimo.