Leviticus 4:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono achotse mafuta ake onse, monga momwe amachotsera mafuta a nsembe yachiyanjano, ndipo wansembe aŵatenthe pa guwalo, kuti atulutse fungo lokomera Chauta. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimo a munthu wamba uja, munthuyo adzakhululukidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka iye achotse mafuta onse monga momwe anachotsera mafuta a chopereka chachiyanjano, ndipo awatenthe pa guwa kuti akhale fungo lokomera Yehova. Potero, wansembe adzapereka nsembe yopepesera tchimo la munthuyo ndipo adzakhululukidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale pfungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhululukidwa.