Leviticus 4:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ngati munthu abwera kudzapereka nkhosa ya nsembe yopepesera machimo, nkhosa yake ikhale yaikazi, yopanda chilema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akadza nayo nkhosa, ndiyo chopereka chake, ikhale nsembe yauchimo, azidza nayo yaikazi, yopanda chilema.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthu apereka mwana wankhosa ngati chopereka chopepesera tchimo lake, abwere ndi mwana wankhosa wamkazi wopanda chilema.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akadza nayo nkhosa, ndiyo copereka cace, ikhale nsembe yaucimo, azidza nayo yaikazi, yopanda cirema.