Leviticus 4:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake wansembe atengeko magazi a nkhosayo ndi chala chake, ndipo aŵapake pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndi kuthira magazi otsalawo patsinde pa guwalo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka wansembe atengeko ndi chala chake magazi a mwana wankhosa uja ndi kuwapaka pa nyanga za guwa lansembe zopsereza. Magazi otsalawo athire pa tsinde la guwalo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wace wonse patsinde pa guwa la nsembe;