Leviticus 4:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake wansembe apakeko magaziwo pa nyanga za guwa la m'chihema chamsonkhano lofukizirapo lubani wonunkhira fungo lokoma pamaso pa Chauta. Magazi ena otsala a ng'ombeyo aŵathire pa tsinde la guwa la nsembe zopsereza, limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la chofukiza cha fungo lokoma, lokhala m'chihema chokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka wansembe apake magaziwo pa nyanga za guwa lofukizira lubani limene lili pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. Magazi ena otsalawo awathire pa tsinde pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pa khomo la tenti ya msonkhano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la cofukiza ca pfungo lokoma, lokhala m'cihema cokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la cihema cokomanako.