Leviticus 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu akaitanidwa ku bwalo la milandu, namlumbiritsa kuti achite umboni wa zinthu zimene adaziwona kapena adazidziŵa, iyeyo nakana kupereka umboniwo, munthu ameneyo ndi woyenera kumlanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati munthu anayitanidwa ku bwalo kuti akachitire umboni pa zimene anaziona kapena kuzimva koma iye nʼkukana kuchitira umboni, munthu ameneyo wachimwa ndipo ayenera kulangidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akacimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osaulula, azisenza mphulupulu yace;