Leviticus 5:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo apereke mbalame inayo kuti ikhale nsembe yopsereza, potsata mwambo wake. Wansembe atachita mwambo wopepesera machimo amene munthuyo wachita, wochimwayo adzakhululukidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aikonze inzake ikhale nsembe yopsereza, monga mwa lemba lake; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa adachimwira, ndipo adzakhululukidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake wansembe apereke mbalame inayo kuti ikhale chopereka chopsereza potsata mwambo wake. Wansembe atatha kupereka nsembe yopepesera tchimo limene munthu uja wachita, wochimwayo adzakhululukidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo aikonze inzace ikhale nsembe yopsereza, manga mwa lemba lace; ndipo wansembe amcitire comtetezera cifukwa ca kucimwa adacimwira, ndipo adzakhululukidwa.