Leviticus 5:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ngati munthu alibe njiŵa ziŵiri kapena nkhunda ziŵiri, abwere ndi ufa wosalala wokwanira muyeso wa kilogaramu limodzi, kuti ukhale nsembe yopepesera tchimo limene wachita. Asathireko mafuta kapenanso lubani, chifukwa imeneyi ndi nsembe yopepesera machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma ngati munthuyo alibe njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri, abweretse ufa wosalala wokwanira kilogalamu imodzi kuti ukhale chopereka chopepesera tchimo limene wachita. Asathiremo mafuta kapena lubani chifukwa ndi chopereka chopepesera tchimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma cuma cace cikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wocimwayo azidza naco copereka cace limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yaucima; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo libona ai; pakuti ndico nsembe yaucimo.