Leviticus 5:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono abwere ndi ufa kwa wansembe, ndipo wansembeyo atapeko wa dzanja limodzi ngati chikumbutso ndi kuutenthera pa guwa, pamodzi ndi nsembe zopereka kwa Chauta. Imeneyi ndiyo nsembe yopepesera machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adze nacho kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale chikumbutso chake, nachitenthe pa guwa la nsembe monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yauchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abweretse ufawo kwa wansembe ndipo wansembeyo atapeko dzanja limodzi kuti ukhale ufa wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa pamodzi ndi chopereka chopsereza kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adze naco kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale cikumbutso cace, nacitenthe pa guwa la nsembe monga umo amacitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yaucimo.