Leviticus 5:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Umu ndimo m'mene wansembe adzachitire mwambo wopepesera munthu amene adachimwa, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. Tsono zotsala zikhale za wansembeyo, monga momwe amachitira ndi chopereka cha chakudya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwira chimodzi cha izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo chotsalira chikhale cha wansembe, monga umo amachitira chopereka chaufacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Umu ndi mmene wansembe adzachitire mwambo wopepesera machimo ena aliwonse amene munthu wachita, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. Zopereka zonse zotsala zidzakhala za wansembeyo monga momwe amachitira ndi chopereka chachakudya.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe amcitire comtetezera cifukwa ca kucimwa kwace adacimwira cimodzi ca izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo cotsalira cikhale ca wansembe, monga umo amacitira copereka caufaco.